Yona 2 - Buku LopatulikaPemphero la Yona ali m'mimba mwa chinsomba 1 Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m'mimba mwa nsombayo. 2 Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga. 3 Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, ndipo madzi anandizinga; mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza. 4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu; koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika. 5 Madzi anandizinga mpaka moyo wanga, madzi akuya anandizungulira, kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu. 6 Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga. 7 Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika. 8 Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao. 9 Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova. 10 Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi