Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yona 2:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adati, “Inu Chauta, pamene ndinali m'mavuto ndidakuitanani, ndipo mudandiyankha. Pamene ndinali m'dziko la akufa ndidalira kwa Inu kuti mundithandize, ndipo mudamva pempho langa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anati: “Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova, ndipo Iye anandiyankha. Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo, ndipo Inu munamva kulira kwanga.

Onani mutuwo Koperani




Yona 2:2
26 Mawu Ofanana  

Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.


Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.


Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.


Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.


Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.


Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.


Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m'dzenje lapansi;


pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,


kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.


pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.


Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.


Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; chifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kuchuluka kwa kudandaula kwanga ndi kuvutika kwanga.


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa