Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 2:8 - Buku Lopatulika

8 Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Anthu opembedza milungu yachabe amataya kukhulupirika kwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe amataya chisomo chawo.

Onani mutuwo Koperani




Yona 2:8
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anakaniza malemba ake, ndi chipangano anachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa.


Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.


Ndikwiya nao iwo akusamala zachabe zonama, koma ndikhulupirira Yehova.


Mundilanditse kuthope, ndisamiremo, ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama.


Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.


Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.


musapatukire inu kutsata zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza zili zopanda pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa