Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yona 2:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu; koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu; koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pamene ndidati, ‘Mwanditaya kutali ndi Inu. Kodi ndidzaiyang'ananso bwanji Nyumba yanu yoyera?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa pamaso panu; komabe ndidzayangʼananso ku Nyumba yanu yopatulika.’

Onani mutuwo Koperani




Yona 2:4
20 Mawu Ofanana  

popeza adzamva za dzina lanu lalikulu ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika kunyumba ino;


ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m'dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, kumzinda munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;


pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.


akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse, m'dziko la undende wao, kumene adawatengera andende; nakapemphera kuloza ku dziko lao limene munapatsa makolo ao, ndi mzinda mudausankha, ndi kunyumba ndamangira dzina lanuyi;


Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.


Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.


Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.


Munandiika kunsi kwa dzenje, kuli mdima, kozama.


Mkwiyo wanu utsamira pa ine, ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Koma Ziyoni anati, Yehova wandisiya ine, ndipo Ambuye wandiiwala ine.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu.


madzi anayenda pamwamba pamutu panga, ndinati, Ndalikhidwa.


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa.


Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.


Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa