Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 2:6 - Buku Lopatulika

6 Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndidatsikira kunsi ndithu, m'tsinde mwa mapiri, kudziko kumene mipiringidzo idanditsekera mpaka muyaya. Koma Inu Chauta, Mulungu wanga, mudanditulutsa kumandako ndili moyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri; mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha. Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo, Inu Yehova Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani




Yona 2:6
25 Mawu Ofanana  

pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati, Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo.


Koma anandiombola ndingatsikire kumanda, ndi moyo wanga udzaona kuunika.


Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi chovala; madzi anafikira pamwamba pa mapiri.


anakwera m'mapiri, anatsikira m'zigwa, kufikira malo mudawakonzeratu.


Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.


Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.


Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Zingwe za manda zindizinga, misampha ya imfa inandifikira ine.


Yehova munabweza moyo wanga kumanda, munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.


M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje? Ngati fumbi lidzayamika Inu? Ngati lidzalalikira choonadi chanu?


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu; pozingidwa nacho chilimbiko.


Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo; ndalowa m'madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.


Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?


pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,


kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.


Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.


Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.


Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.


Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa