Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 4:7 - Buku Lopatulika

7 Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Ansembe ankati akamachulukirachulukira, ndi m'menenso ankanyanyira kundichimwira. Ndidzasandutsa ulemu wao kuti ukhale manyazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ansembe ankati akachuluka iwo ankandichimwiranso kwambiri; iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 4:7
15 Mawu Ofanana  

Chiyambire masiku a makolo athu tapalamula kwakukulu mpaka lero lino; ndi chifukwa cha mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kuchitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino.


Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.


Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake.


Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.


Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; chifukwa chake anandiiwala Ine.


Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova.


Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.


Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha panjira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.


Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.


Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; chikho cha dzanja lamanja la Yehova chidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako.


Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.


Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa