Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 8:11 - Buku Lopatulika

11 Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Oweruza akamachedwetsa chilango cha anthu opalamula, anthu ena amalimba mtima nkumafuna kuti ayambe kuchita zoipa nawonso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pamene chigamulo cha anthu opalamula mlandu chikuchedwa, mitima ya anthu imadzaza ndi malingaliro ochita zolakwa.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:11
19 Mawu Ofanana  

Ndi m'kalatamo analemba kuti, Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mumlekerere kuti akanthidwe nafe.


Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo; koma maso ake ali panjira zao.


Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.


Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine; ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine.


Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.


Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;


Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalole anthu amuke.


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.


Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?


chifukwa chake mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe mu Ejipito, kukakhala m'menemo;


Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa