Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 58:1 - Buku Lopatulika

1 Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Kodi mumagamuladi molungama, inu akuluakulu oweruza? Kodi mumaweruzadi anthu mwachilungamo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama? Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 58:1
18 Mawu Ofanana  

Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.


Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.


Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.


Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga, ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.


Taonani mfumu idzalamulira m'chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'chiweruzo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.


Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;


Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa