Ndikufuna ndikuuzeni, sikulakwa kukhala ndi malo ochezera, chifukwa zimatithandiza kulankhulana ndi okondedwa athu akutali. Koma cholakwika ndi kugwiritsa ntchito molakwika, kuipitsa mzimu, maganizo ndi moyo wathu ndi zomwe timafuna kapena kugawana. Tiyeni tisamale ndi zomwe tikuona, kumva ndi kulemba, chifukwa maso a Mulungu ali pa ife ndipo amafuna kuti tikhale olungama m'njira zathu zonse.
Lero ndikukulimbikitsani kuti mukhale kuunika, osatsata mafunde a dziko, koma mukhale osiyana m'zonse zomwe mumachita. Lolani aliyense amene akukutsatirani asangalale ndi uthenga wabwino ndipo alimbikitsidwe ndi zomwe mumayika pa Facebook yanu.
Komanso, chotsani akaunti iliyonse yomwe siyipindulitsa pa moyo wanu. Musatsatire masamba omwe amawononga mtima wanu, makhalidwe ndi mfundo zanu. Malo alionse ochezera omwe muli nawo ayenera kuwonetsa Khristu, ndipo zimenezo zidzalankhula zokha za zomwe zili mumtima mwanu.
Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.
woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.
Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake.
Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;
Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.
Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,