Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 3:13 - Buku Lopatulika

13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 3:13
15 Mawu Ofanana  

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;


koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.


Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;


Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.


Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,


Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,


Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa