Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.
Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.
osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.
M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?
Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo.
Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.
ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;
Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.
kuti kusakhale chisiyano m'thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake.
Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.
Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu.
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,
Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.
Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.
Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.
kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.
koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.
koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai;
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;
Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.
Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.
Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:
Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;
Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Ndipo chisomo chake cha Ambuye Mulungu wathu chikhalire pa ife; ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu; inde, ntchito ya manja athu muikhazikitse.
Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.