Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 12:12 - Buku Lopatulika

12 Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 12:12
16 Mawu Ofanana  

Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.


Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi.


Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.


Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.


Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.


amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m'zonse.


kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;


Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu;


Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.


pakuti tili ziwalo za thupi lake.


Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.


Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;


kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.


Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa