Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
Masalimo 1:1 - Buku Lopatulika Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza. |
Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira.
Chikukomerani kodi kungosautsa, kuti mupeputsa ntchito yolemetsa manja anu, ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.
Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.
Ndipo ndinati kwa ana ao m'chipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;
Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.
(amene sanavomereze kuweruza kwao ndi ntchito yao) wa ku Arimatea, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu,
Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaone.
amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.
Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.
Ndipo nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya.
Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.
Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.