Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero


BUKU LOYAMBA Masalimo 1–41 Salimo 1

1 Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.

2 Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.

3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.

4 Sizitero ndi anthu oyipa! Iwo ali ngati mungu umene umawuluzidwa ndi mphepo.

5 Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo, kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.

6 Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama, koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.

The Word of God in Contemporary Chichewa

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®

Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®

Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Biblica, Inc.
Titsatireni:



Zotsatsa