Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 10:3 - Buku Lopatulika

3 Chikukomerani kodi kungosautsa, kuti mupeputsa ntchito yolemetsa manja anu, ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Chikukomerani kodi kungosautsa, kuti mupeputsa ntchito yolemetsa manja anu, ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kodi inu zikukukomerani kuti mundizunze ndi kundinyoza ine, ntchito ya manja anune, chonsecho mukukondera upo wa anthu oipa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kodi mumakondwera mukamandizunza, kunyoza ntchito ya manja anu, chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa?

Onani mutuwo Koperani




Yobu 10:3
27 Mawu Ofanana  

Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu, koma mufuna kundiononga.


Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.


Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, ndi kulola mau otere atuluke m'kamwa mwako.


Mulungu andipereka kwa osulangama, nandiponya m'manja a oipa.


Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga, nandizinga ndi ukonde wake.


Taonani, zokoma zao sizili m'dzanja lao; (koma uphungu wa oipa unditalikira.)


Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino; koma uphungu wa oipa unditalikira.


Pali Mulungu, amene anandichotsera zoyenera ine, ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,


Mwasandulika kundichitira nkharwe; ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.


Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenge iyenso? Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?


Mzimu wa Mulungu unandilenga, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.


Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse? Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.


Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?


Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro; kapena kugwiriziza ochita zoipa.


Kuli chimodzimodzi monsemo, m'mwemo ndikuti Iye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi.


Dziko lapansi laperekedwa m'dzanja la woipa; aphimba maso a oweruza ake. Ngati sindiye, pali yaninso?


Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.


Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.


Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake.


Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.


Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa