Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 22:3 - Buku Lopatulika

3 Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Iyeyonso ankatsata chitsanzo cha banja la Ahabu, poti mai wake ndiye ankamupatsa uphungu woipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Nayenso anayenda mʼnjira ya banja la Ahabu, pakuti amayi ake anamulimbikitsa kuchita zolakwika.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 22:3
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anayenda m'njira ya nyumba ya Ahabu, nachita choipa pamaso pa Yehova, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa chibale cha banja la Ahabu.


Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu chaka chimodzi; ndi dzina la make ndiye Ataliya mwana wa Omuri.


Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wake; ndi kuonongeka kwake nkumeneko.


Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.


Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola chitseko cha nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.


koma anayenda m'njira za mafumu a Israele, napangiranso Abaala mafano oyenga.


Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.


Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.


Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa