Ndipo ine ndikukuuzani, taganizirani izi: Yesu anavulera mabala athu, anapsinjika chifukwa cha machimo athu. Chilango chimene chatibweretsera mtendere chinagwera pa Iye, ndipo ndi zilonda zake ife tachiritsidwa. (Yesaya 53:5) Mukamvetsa zimenezi, mudzadziwa kuti Yesu analipira kale mtengo wa matenda athu, ndipo mwa Iye ife tiri athanzi kale.
Iye anatipatsa mphamvu kuti matenda achoke, monga momwe akunenera mu Marko 16:18, kuti "adzaika manja awo pa odwala, ndipo adzachira." Ndipo tiona kuti sakunena za matenda enaake, koma matenda onse. Choncho ngati mukuvutika ndi chinachake, dzuka ndi chikhulupiriro ndipo uuze matendawa kuti achoke m'dzina la Yesu.
Kulikonse kumene muli, imbirani magazi a Khristu pa inu. Ngakhale makolo anu kapena agogo anu anali ndi matenda omwo, Mulungu wakupatsani mphamvu yoti musiye zimenezo. Chifuniro cha Mulungu pa moyo wanu si chakuti mudwale, Iye akufuna kuti mukhale wathanzi ndipo muzitha kuchiritsa ena.
Kudzera mu kuchiritsidwa kwanu, banja lanu lidzakhulupirira mwa Iye ndipo dzina lake lidzakwezedwa. Dzitsimikizireni kuti ndinu omasuka ku zimene zinkakuponderezani ndipo konzekerani kuona Mulungu akuchiritsa osati thupi lanu lokha, komanso mtima wanu.
Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe.
Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.
Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.
Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.
adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira.
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse;
Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.
Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.
Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse; kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.
Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; chifukwa anatcha iwe wopirikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna.
Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse;
Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lao lonse.
Pamenepo afuulira kwa Yehova m'kusauka kwao, ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao. Atere oomboledwa a Yehova, amene anawaombola m'dzanja la wosautsa; Atumiza mau ake nawachiritsa, nawapulumutsa ku chionongeko chao.
Pamenepo afuulira kwa Yehova m'kusauka kwao, ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao. Atere oomboledwa a Yehova, amene anawaombola m'dzanja la wosautsa; Atumiza mau ake nawachiritsa, nawapulumutsa ku chionongeko chao. Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!
Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye:
Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.
Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.
Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu. ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.
Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.
Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu. Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire. Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima. Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova. Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa. Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede. Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova. Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga. Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga. Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.
Ndipo Iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.
Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu. Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu.
Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa; mitsempha yako idzalandirapo moyo, ndi mafupa ako uwisi.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.
Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani, monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.
Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino. Mkazi aphunzire akhale wachete m'kumvera konse. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete. Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva; ndipo Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa; koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso. chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Muwerenga kuthawathawa kwanga, sungani misozi yanga m'nsupa yanu; kodi siikhala m'buku mwanu?
Ndimkonda, popeza Yehova amamva mau anga ndi kupemba kwanga. Ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ndinazunzika kwambiri. Pofulumizidwa mtima ndinati ine, anthu onse nga mabodza. Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira? Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya okondedwa ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova. Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse. M'mabwalo a nyumba ya Yehova, pakati pa inu, Yerusalemu. Aleluya. Popeza amanditcherera khutu lake, chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse.
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova, ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga. Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo;
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.
Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero, kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo. Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.
Odala angwiro m'mayendedwe ao, akuyenda m'chilamulo cha Yehova. Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa, kuti ndisamalire mau anu. Sindinapatukane nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa. Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga. Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo. Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga. Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama. Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu. Oipa ananditchera msampha; koma sindinasokere m'malangizo anu. Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga. Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu, kosatha, kufikira chimaliziro. Ndidana nao a mitima iwiri; koma ndikonda chilamulo chanu. Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu. Mundichokere ochita zoipa inu; kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga. Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa. Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa, ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire. Mupepula onse akusokera m'malemba anu; popeza chinyengo chao ndi bodza. Muchotsa oipa onse a padziko lapansi ngati mphala: Chifukwa chake ndikonda mboni zanu. Inu ndinu wodala Yehova; ndiphunzitseni malemba anu. Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu. Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo; musandisiyira akundisautsa. Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere; odzikuza asandisautse. Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu, ndi mau a chilungamo chanu. Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu, ndipo ndiphunzitseni malemba anu. Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni; kuti ndidziwe mboni zanu. Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu; pakuti anaswa chilamulo chanu. Chifukwa chake ndikonda malamulo anu koposa golide, inde golide woyengeka. Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga. Mboni zanu nzodabwitsa; chifukwa chake moyo wanga uzisunga. Ndinafotokozera ndi milomo yanga maweruzo onse a pakamwa panu. Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa. Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu; popeza ndinakhumba malamulo anu. Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo, monga mumatero nao akukonda dzina lanu. Khazikitsani mapazi anga m'mau anu; ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse. Mundiombole kunsautso ya munthu: Ndipo ndidzasamalira malangizo anu. Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu; ndipo mundiphunzitse malemba anu. Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu. Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika. Mboni zanuzo mudazilamulira zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu. Changu changa chinandithera, popeza akundisautsa anaiwala mau anu. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse. Mau anu ngoyera ndithu; ndi mtumiki wanu awakonda. Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu. Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha; mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; ndidzasunga malemba anu. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni, ndipo ndidzasamalira mboni zanu. Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu. Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu. Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu; mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova. Ndidzalingirira pa malangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu. Otsata zachiwembu andiyandikira; akhala kutali ndi chilamulo chanu. Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi. Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, kuti munazikhazika kosatha. Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse; pakuti sindiiwala chilamulo chanu. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; mundipatse moyo monga mwa mau anu. Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu. Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu. Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri; koma sindinapatukane nazo mboni zanu. Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu. Penyani kuti ndikonda malangizo anu; mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu. Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha. Nduna zinandilondola kopanda chifukwa; koma mtima wanga uchita nao mantha mau anu. Ndikondwera nao mau anu, ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri. Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo; koma ndikonda chilamulo chanu. Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, chifukwa cha maweruzo anu olungama. Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa. Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova, ndipo ndinachita malamulo anu. Moyo wanga unasamalira mboni zanu; ndipo ndizikonda kwambiri. Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; popeza njira zanga zonse zili pamaso panu. Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova; mundizindikiritse monga mwa mau anu. Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndidzasamalira mau anu. Kupemba kwanga kudze pamaso panu; mundilanditse monga mwa mau anu. Milomo yanga itulutse chilemekezo; popeza mundiphunzitsa malemba anu. Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama. Dzanja lanu likhale lakundithandiza; popeza ndinasankha malangizo anu. Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa. Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani; ndipo maweruzo anu andithandize. Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu. Munditsegulire maso, kuti ndipenye zodabwitsa za m'chilamulo chanu. Ine ndine mlendo padziko lapansi; musandibisire malamulo anu. Odala iwo akusunga mboni zake, akumfuna ndi mtima wonse;
Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;
Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso; ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
Kodi mudzachitira akufa zodabwitsa? Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani? Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi, chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko? Zodabwitsa zanu zidzadziwika mumdima kodi, ndi chilungamo chanu m'dziko la chiiwaliko?
Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.