Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 30:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta, Mulungu wanga, ndidalirira Inu kuti mundithandize, ndipo mwandichiritsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 30:2
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana.


Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai.


Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.


Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.


Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu, Yehova Mulungu wanga; ndipo asandisekerere ine.


Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.


Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera, kuti mafupawo munawathyola akondwere.


Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.


Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova, ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.


ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa