Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 30:1 - Buku Lopatulika

1 Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa, ndipo simunandikondwetsere adani anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa, ndipo simunandikondwetsera adani anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa. Simudalole kuti adani anga akondwere poona kuti ndikuvutika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 30:1
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi aang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.


Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.


Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.


Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!


mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga.


Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.


Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.


kuti anganene mdani wanga, Ndamgonjetsa; ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine.


Yehova, musampatse woipa zokhumba iye; musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze.


Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.


Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, ndisachite manyazi; adani anga asandiseke ine.


Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.


Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu; muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.


Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.


Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine, popeza mdani wanga sandiseka.


Ndinamfuulira Iye pakamwa panga, ndipo ndinamkuza ndi lilime langa.


Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu.


Takhala chotonza cha anansi athu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.


Onse opita panjira akuombera manja: Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati, kodi uwu ndi mzinda wotchedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?


Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.


Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa