Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Yesu adayendera mizinda ndi midzi yonse. Adanka naphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, nkumalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wakumwamba. Ndiponso ankachiritsa nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:35
12 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.


Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'mizinda mwao.


akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,


Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.


Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa