Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 6:10 - Buku Lopatulika

10 Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwechonso pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 6:10
44 Mawu Ofanana  

Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.


Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.


Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.


Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.


Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake.


Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.


Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.


Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.


nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.


Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.


Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide; Hosana mu Kumwambamwamba.


Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.


Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.


nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere mu Mwamba, ndi ulemerero mu Mwambamwamba.


nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike.


Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.


Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.


Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.


Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.


Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kuchitidwe.


Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake.


Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.


si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;


amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;


Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,


Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama;


M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.


pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.


akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.


Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa;


kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Ndipo ndinamva mau aakulu mu Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.


Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.


Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa