Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 4:2 - Buku Lopatulika

2 Chitani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Chitani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 4:2
21 Mawu Ofanana  

Zedi uyesa chabe mantha, nuchepsa chilingiriro pamaso pa Mulungu.


M'malo mwa chikondi changa andibwezera udani; koma ine, kupemphera ndiko.


Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.


Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake.


Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;


Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.


Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.


kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.


mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.


Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,


ozika mizu ndi omangiririka mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.


Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.


Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.


Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbika m'mapemphero ake masiku onse chifukwa cha inu, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake.


Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa