Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 4:3 - Buku Lopatulika

3 ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 4:3
27 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.


Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.


Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,


Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.


Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.


Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,


Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,


ndi umo anandizindikiritsa chinsinsicho mwa vumbulutso, monga ndinalemba kale mwachidule,


chimene mukhoza kuzindikira nacho, pakuchiwerenga, chidziwitso changa m'chinsinsi cha Khristu,


ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse;


Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,


Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;


monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.


ndiwo chinsinsicho chinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake,


Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu.


Abale, tipempherereni ife.


Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachite manyazi ndi unyolo wanga;


m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.


lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.


Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa