Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m'Baibulo Okhudza Kupanda Kuleza Mtima

110 Mau a m'Baibulo Okhudza Kupanda Kuleza Mtima

Nthawi zambiri timafuna zinthu mwachangu, timafuna mayankho msanga komanso njira zopezera mavuto athu popanda kudikira. Koma inu, mukuona bwanji? Kodi nthawi zina simukhumudwa mukadzayembekezera?

Baibulo limatiphunzitsa zambiri pankhani yokhala oleza mtima. Monga mmene Salimo 37:7 limatiuza, "Khalani chete pamaso pa Yehova, ndipo muzikhala moleza mtima m’kumuyembekezera. Musakwiye chifukwa cha munthu amene akuchita bwino pa moyo wake, chifukwa cha munthu amene akuchita zinthu zopanda pake." Tiyeni tiziyesetsa kukhala chete pamaso pa Mulungu ndikumuyembekezera moleza mtima.

Kumbukirani nkhani ya Abrahamu ndi Sara. Iwo anayembekezera nthawi yaitali kuti akhale ndi mwana. Ngakhale kuti zinatenga nthawi yaitali, Mulungu anakwaniritsa lonjezo lake ndipo anawapatsa mwana pa nthawi yake yoyenera. Zimenezi zimatiphunzitsa kuti zolinga za Mulungu nthawi zina sizigwirizana ndi zomwe ife timaganiza, koma tingadalire chikondi chake ndi nzeru zake. Kodi simukuganiza kuti nkhani ya Abrahamu ndi Sara ndi yolimbikitsa?

Timakumana ndi vuto la kusaleza mtima tsiku ndi tsiku, koma Baibulo limatipatsa njira zothanirana nalo. Timaphunzira kudalira Ambuye, kukhala moleza mtima ndikuyembekezera nthawi yake, komanso kukumbukira kuti zolinga zake ndi zazikulu kuposa malingaliro athu. Ndikukhulupirira kuti inuyo mudzapeza mphamvu mwa Mulungu kuti mukhale oleza mtima.




Masalimo 37:7

Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:40

Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 32:1

Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:13

Koma anaiwala ntchito zake msanga; sanalindire uphungu wake:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19-20

Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 21:4

Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:29

Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 14:29

Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 4:8-9

Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai. Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:7-8

Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika. Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:14

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:32

Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:2-4

Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi. pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4

Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:36

Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:9

Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:2

ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:7-9

Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu. Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa. Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:25

Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:12

kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:1

Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:9

Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 14:14

Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 3:25-26

Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:8

Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:5

Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira, ndiyembekeza mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:3-4

pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:18

Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:24

Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:5

Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:5-6

Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:7

kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:10-11

Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:24

Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:18

Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:14

Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:34

Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:22

Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:15

Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:20-21

Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu. Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:5

Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:4-6

koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja, m'mikwingwirima, m'ndende, m'maphokoso, m'mavutitso, m'madikiro, m'masalo a chakudya; m'mayeredwe, m'chidziwitso, m'chilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'chikondi chosanyenga;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 123:2

Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:23

Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:11

olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:3

ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:15

Chipiriro chipembedza mkulu; lilime lofatsa lithyola fupa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31-32

Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:3

Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:9

Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:2-4

amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa; kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:16

Mkwiyo wa chitsiru udziwika posachedwa; koma wanzeru amabisa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:5-6

Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi. Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:19

Mudzakhala nao moyo wanu m'chipiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:20

Moyo wathu walindira Yehova; Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:16

komatu mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:5-6

Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:11

Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:18

Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 49:18

Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:24

Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:10

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:28

Wosalamulira mtima wake akunga mzinda wopasuka wopanda linga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:1

Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:25

Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14-15

Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:9

osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 64:4

Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:10

Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:4

Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:34

Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:17-18

Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso. Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:6-7

Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:8

Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:8

Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:13-14

Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani! Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:10

Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:13-14

Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:13

Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:27-28

Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 3:12-13

koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu; kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:27

Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:7

(Pakuti tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe);

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:20-21

Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu, akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:25

Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:2

lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:15

Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:8-9

Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, ndi mzimu wanga wonse, nzeru zanga zonse, ndi moyo wanga wonse, ndikulemekeza dzina lanu ndi kukupatsani ulemerero. Mulungu wanga akwezedwe kwamuyaya, chifukwa ndi wabwino, wolungama, wachifundo, palibe wina wofanana naye, palibe wina woyerekezeka naye. Ndinu Mulungu wa chipulumutso changa, chiyembekezo changa, amene amabwezeretsa ndi kuchiritsa moyo wanga. Ndimakukhulupirirani ndi kudalira mphamvu yanu kuti mundithandize pa zosowa zanga zonse. Lero ndikupemphani kuti mundithandize m'nthawi ya kusatsimikiza ndi kuyembekezera, ndikulakalaka chitsogozo chanu Ambuye. Ndikupempha modzichepetsa pamaso panu, kuti mundimasule ku kusaleza mtima komwe kumandiwononga ndi kundilepheretsa kukhala chete. Mundipatse mtendere wanu kuti ndikhulupirire chifuniro chanu ndi mphamvu zoyembekezera moleza mtima kukwaniritsidwa kwa malonjezano anu. Ndidzipereka m'manja mwanu achikondi, ndikukhulupirira kuti nzeru zanu ndi chikondi chanu zinditsogolera panjira yoyenera. Inu Mulungu, mundimasule kwathunthu ku khalidwe losaleza mtima ndi kundiphunzitsa kupumula mokwanira m'nthawi yanu yoyenera. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa