Taganizirani kuti zonse zomwe muli nazo ndi mphatso yochokera ku chisomo cha Mulungu: malo amene mwafikira, banja lanu, nyumba yanu, ndi luso lanu lonse, zonsezi Mulungu ndiye anaziyika m'moyo mwanu, si chifukwa cha mphamvu zanu kapena nzeru zanu, koma chifukwa cha chifundo chake.
Choncho, musadzitame chifukwa cha nzeru zanu kapena kudziona kuti ndinu wodzidalira, ndipo musalole kuti mtima wanu uipitsidwe ndi chuma chanu.
M'malo mwake, tumikirani Yesu ndi zonse zomwe muli nazo, musamakane kuthandiza osowa ndi kupatsa malo akazi amasiye; khalani dalitso lochokera kwa Mulungu kwa anthu omwe akuzungulirani.
Mulungu amadalitsa wopereka mokondwera ndipo sakhala mopanda pake m'dziko lino.
Samalirani ndipo khalani odzipereka chifukwa chomwe chikukusamalirani lero chingakuphekani mawa ngati simukuchidziwa kuchigwiritsa ntchito bwino.
Ndalama sizili zoti tichite zoipa kapena kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika, koma zoti tithandizire, tipange zinthu zabwino, ndi kukhala yankho la zosowa za anthu.
Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.
Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.
Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;
Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.
Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda.
polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.
Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.
Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;
Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.
Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, ndipo anadya zipatso za m'minda; namyamwitsa uchi wa m'thanthwe, ndi mafuta m'mwala wansangalabwe; mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa, ndi mafuta a anaankhosa, ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde, ndi impso zonenepa zatirigu; ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa. Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.
Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji. Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.
Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.
Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.
Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao. ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.
Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo; kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.
Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.
Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga. Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.
Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu! Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.
Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe. Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse. Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo. Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu. Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro. Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa? Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani? Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo. Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga. Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira. Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa; Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe? Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe? Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina? Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa. ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga; kodi simunasiyanitse mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?
Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?
M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.
Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.
Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko.
Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao; inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikira iwo ndi zinthu zathupi.
Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa; koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?
Iwo akutama kulemera kwao; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao; kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu. Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthawi zonse.
Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse. Pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.
Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona?
Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.
Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.
Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, chabwino nchiti ndichichite, kuti ndikhale nao moyo wosatha? Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo. Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Ndipo makamu aakulu a anthu anamtsata; ndipo Iye anawachiritsa kumeneko. Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani? Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate. Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.
Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.
Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo: iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa; makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.
chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira. Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;
Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.
Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.
Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho.
Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.
Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu. Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.
Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho. Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.
Zinthu ziwiri ndakupemphani, musandimane izo ndisanamwalire: Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika. Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa. M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.
ndipo mbale wolemera anyadire pamene atsitsidwa, pakuti adzapita monga duwa la udzu. Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.
Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.
Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera.
Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.
Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?
Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.
Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.
Usadye zakudya zake za wa maso ankhwenzule, ngakhale kukhumba zolongosoka zake. Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, Idya numwe; koma mtima wake suli pa iwe.
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?
Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.
podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu:
Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli. Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu. Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka. Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wake kwambiri; chifukwa Mulungu amvomereza m'chimwemwe cha mtima wake.
Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu.
chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.