Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 9:14 - Buku Lopatulika

14 Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Momwemonso Ambuye adalamula kuti olalika Uthenga Wabwino, azilandira zoŵasunga pakulalika Uthengawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Chomwechonso Ambuye akulamula kuti wolalikira Uthenga Wabwino azilandira thandizo lawo polalikira Uthenga Wabwinowo.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 9:14
13 Mawu Ofanana  

kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.


Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba.


Ndipo m'mudzi uliwonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani;


ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema.


Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.


Ngati takufeserani inu zauzimu, kodi nchachikulu ngati ife tituta za thupi lanu?


Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.


Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.


Kodi tilibe ulamuliro wa kudya ndi kumwa?


Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa