1 Akorinto 9:15 - Buku Lopatulika15 Koma ine sindinachite nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Koma ine sindinachita nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Koma ineyo sindinkagwiritsa ntchito konse lamulo limeneli. Ndiponso sindikulemba kalatayi chifukwa chofuna kuligwiritsa ntchito kumene. Kwenikweni ndikadakonda kuti ndife, kupambana kuti wina andichotsere chifukwa chimene ndimanyadira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Koma ine sindinagwiritse ntchito ufulu woterewu. Sindikulemba izi ndi chiyembekezo choti mundichitire zoterezi. Kuli bwino ndife kusiyana nʼkuti wina alande zomwe ndimazinyadira. Onani mutuwo |