Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 9:13 - Buku Lopatulika

13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za m'Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kodi simudziŵa kuti otumikira m'Nyumba ya Mulungu, amadya chakudya cha m'Nyumbamo, ndipo kuti opereka nsembe pa guwa lansembe, amalandira nao zansembezo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kodi simukudziwa kuti wogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amapeza chakudya chawo mʼNyumbamo, ndipo kuti otumikira pa guwa lansembe amagawana zimene zaperekedwa pa guwa lansembelo.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 9:13
15 Mawu Ofanana  

Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;


Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.


Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako.


Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo paguwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake.


Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako.


Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?


Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?


Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.


Chifukwa chake Levi alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi abale ake; Yehova mwini wake ndiye cholowa chake, monga Yehova Mulungu wake ananena naye.


Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa