1 Akorinto 9:12 - Buku Lopatulika12 Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachita nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Ngati ena adziyesa kuti ndi oyenera kulandira zimenezi kwa inu, nanga ife sindiye oyenera koposa iwowo kuzilandira? Komabe kuyenera kumeneku sitidakugwiritse ntchito ai. Makamaka tidapirira zonse, kuwopa kuti tingachedwetse anthu mwa njira iliyonse kulandira Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Ngati ena ali ndi ufulu wothandizidwa ndi inu, kodi ife sitikuyenera kukhala nawo ufulu ochulukirapo? Koma ife sitinagwiritse ntchito ufulu umenewu. Mʼmalo mwake timangodzichitira chilichonse posafuna kutsekereza ena kumva Uthenga Wabwino wa Khristu. Onani mutuwo |