Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Luka 16:10 - Buku Lopatulika

10 Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.

Onani mutuwo Koperani

Luka 16:10
9 Mawu Ofanana  

Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?

Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.

Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.

Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa mizinda khumi.

Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.

Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,

Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.

amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yake yonse.

Titsatireni:

Zotsatsa

Zotsatsa