Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 5:11 - Buku Lopatulika

11 Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Chuma chikachuluka, odya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani? Si kumangoziyang'ana basi?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Chuma chikachuluka akudya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani kuposa kumangochiyangʼana ndi maso ake?

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 5:11
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamira.


Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide.


Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.


Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.


Ndinakula chikulire kupambana onse anali mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.


Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.


Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.


Taonani, sichichokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto ntchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pake?


Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa