Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 1:11 - Buku Lopatulika

11 Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Dzuŵa limatuluka nkutentha kwake, ndipo limaumitsa udzu. Duŵa la udzuwo limathothoka, kukongola kwake nkutha. Chomwechonso moyo wa wolemerayo udzazimirira ali pakati pa zochita zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 1:11
27 Mawu Ofanana  

Alendo adzafota, nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.


Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu.


Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga.


Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo.


Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Mamawa uphuka bwino; madzulo ausenga, nuuma.


Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake.


Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.


ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake.


Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.


Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.


nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.


Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?


ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.


ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.


kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,


Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa