Ndikufuna ndikuuzeni za ubwenzi weniweni. Uwu ndi ubwenzi umene umakhalapo ngakhale ena onse atathawa. Si munthu amene mumaonana naye tsiku ndi tsiku, koma ndi amene amapezeka pa nthawi zovuta. Si amene amakutumizirani mauthenga nthawi zonse, koma amene amakutumizirani uthenga woyenera pa nthawi yoyenera, ngati akudziwa kuti mukuvutika.
Ubwenzi unayambira kwa Mulungu kuti tizilimbikitsana, pakuti awiri aposa m'modzi. Nthawi zina, chomwe mukufuna ndi kungocheza ndi mnzako, macheza amene angakumasuleni ndi kukutonthozani, chinthu chimene mungagawane ndi amene mumawadalira.
Ndikukulimbikitsani kuti mukhale mnzake amene mukufuna kukhala naye, mupereke chikondi chimene mukufuna kulandira. Mulungu akufuna kukugwiritsani ntchito kutonthoza mnzake amene akuvutika. Mupite mukamuchezere, mulole Mulungu amukumbatire kudzera mwa inu, mumumvetsere popanda kumuweruza ndipo mukamachoka muzipempherera.
Muziwalimbikitsa ndi mawu a Mulungu mpaka atapezanso chimwemwe mumtima mwake. Musanyalanyaze mavuto awo, chifukwa anthu ambiri amasankha kuvutika okha. Ntchito yanu ndi kukhala wolimbikitsa amene angadalire, musamusiye, musalole choipa chimuvutitse.
Dzazani mtima wanu ndi chifundo, ngakhale simukumvetsa, kungokhalapo n'kokwanira, ngakhale mutakhala chete. Muwapukutire misozi, muwasonyeze chikondi cha Mulungu ndipo khalani nawo mpaka utawaleza utawonekere pa mitambo yawo yakuda. Kumbukirani mwambi woti: "Nthawi zonse uzikonda mnzanu, ndipo iye adzakhala ngati m'bale wanu pa nthawi ya masautso" (Miyambo 17:17). Ngakhale atakhala kuti alibe banja lake, Mzimu Woyera akufuna kudziwonetsera kudzera mwa inu.
Musadandaule kuti mungakambe chiyani, Iye adzakupatsani mawu ndi kukuyikani mkamwa mwanu zimene mnzako akufunikira mumtima mwake.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.
Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.
Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka.
Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu. Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti? Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.
Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala? Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala.
Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira. Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi, kumliri wosakaza. Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.
Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.
Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.
Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.
(pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);