Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 6:2 - Buku Lopatulika

2 (pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 (pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Paja Mulungu akuti, “Pa nthaŵi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima, ndidakumvera, pa nyengo ya kupulumutsa anthu, ndidakuthandiza.” Mvetsani, ndi inotu nthaŵi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi Lerotu tsiku la chipulumutsolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pakuti akunena kuti, “Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera, ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza. Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 6:2
10 Mawu Ofanana  

Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.


Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;


ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;


Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.


Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye.


komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;


Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake,


alangizanso tsiku lina, ndi kunena mu Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa