Masalimo 102 - Buku LopatulikaWopsinjika apempha Mulungu achitire anthu ake chifundo, amitundu nammverenso Pemphero la Wozunzika, m'mene anakomoka natsanulira cholingalira chake pamaso pa Yehova. 1 Yehova, imvani pemphero langa, ndipo mfuu wanga ufikire Inu. 2 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga. 3 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi, ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni. 4 Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga. 5 Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga. 6 Ndikunga vuwo m'chipululu; ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja. 7 Ndidikira, ndikhala ngati mbalame ili yokha pamwamba pa tsindwi. 8 Adani anga anditonza tsiku lonse; akundiyalukirawo alumbirira ine. 9 Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate, ndi kusakaniza chomwera changa ndi misozi, 10 chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu; popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa. 11 Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu. 12 Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse; ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo. 13 Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika. 14 Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yake, nachitira chifundo fumbi lake. 15 Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova, ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu. 16 Pakuti Yehova anamanga Ziyoni, anaoneka mu ulemerero wake; 17 anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao. 18 Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova. 19 Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ake opatulika; Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi; 20 kuti amve kubuula kwa wandende; namasule ana a imfa. 21 Kuti anthu alalikire dzina la Yehova mu Ziyoni, ndi chilemekezo chake mu Yerusalemu; 22 Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu, ndi maufumu kuti atumikire Yehova. 23 Iye analanda mphamvu yanga panjira; anachepsa masiku anga. 24 Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga: Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo. 25 Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu. 26 Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika: 27 Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizifikira kutha. 28 Ana a atumiki anu adzakhalitsa, ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi