Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:18 - Buku Lopatulika

18 Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mbadwo wakutsogolo, kuti anthu amene mpaka tsopano lino sanabadwebe, nawonso adzatamande Chauta,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo, kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:18
21 Mawu Ofanana  

Penyetsetsani malinga ake, yesetsani zinyumba zake; kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.


Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze, nyanja ndi zonse zoyenda m'mwemo.


Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.


anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.


yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.


chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.


koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.


Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.


Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.


Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira izi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa