Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:17 - Buku Lopatulika

17 anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Adzayankha pemphero la anthu ake otayika, sadzanyoza kupemba kwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:17
16 Mawu Ofanana  

Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.


mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.


Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeretsa; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, mu Yerusalemu.


Yehova amanga Yerusalemu; asokolotsa otayika a Israele.


Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.


M'maso mwao mude, kuti asapenye; ndipo munjenjemeretse m'chuuno mwao kosalekeza.


Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi.


Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.


ndipo ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena chomwecho.


Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mzindawu udzamangidwira Yehova kuyambira pa Nsanja ya Hananele kufikira ku Chipata cha Kungodya.


Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.


Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa