Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:5 - Buku Lopatulika

5 Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndaonderatu ngati munthu wachitopa, ntchito yanga ndi kubuula nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:5
10 Mawu Ofanana  

Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.


Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.


Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.


Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.


Mamawa uphuka bwino; madzulo ausenga, nuuma.


Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.


Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala; khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.


Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa