Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:4 - Buku Lopatulika

4 Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mtima wanga wakanthidwa, ndipo wafota ngati udzu, zoonadi, ngakhale chakudya chimandinyansa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu; ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:4
21 Mawu Ofanana  

Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.


Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya Mulungu, nalowa m'chipinda cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadye mkate, sanamwe madzi; pakuti anachita maliro chifukwa cha kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.


Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.


Khungu langa lada, nilindifundukira; ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.


M'mwemo mtima wake uchita mseru ndi mkate, ndi moyo wake pa chakudya cholongosoka.


Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.


Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu.


Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate, ndi kusakaniza chomwera changa ndi misozi,


Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.


Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.


Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.


Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika; ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.


udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.


Walasa impso zanga ndi mivi ya m'phodo mwake.


Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine.


Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadye kapena kumwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa