Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:11 - Buku Lopatulika

11 Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Masiku anga ali pafupi kutha ngati mthunzi wamadzulo. Ndikufota ngati udzu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo; Ine ndikufota ngati udzu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:11
12 Mawu Ofanana  

Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.


Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu; nachizula chiyembekezo changa ngati mtengo.


Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.


Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira.


Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?


Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake.


ndipo mbale wolemera anyadire pamene atsitsidwa, pakuti adzapita monga duwa la udzu.


inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.


Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa