Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:26 - Buku Lopatulika

26 Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Zonsezi zidzatha ngati malaya, koma Inu mulipobe. Inu mumazisintha ngati chovala, ndipo zimatha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo; zidzatha ngati chovala. Mudzazisintha ngati chovala ndipo zidzatayidwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:26
14 Mawu Ofanana  

Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.


Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse; ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo.


Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.


Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.


Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi padziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.


Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.


Pakuti monga m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.


Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa