Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:24 - Buku Lopatulika

24 Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga: Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga: Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Ndikuti, “Mulungu wanga, musandichotse tsopano ndisanakalambe, Inu amene zaka zanu sizitha mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Choncho Ine ndinati: “Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga; zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:24
10 Mawu Ofanana  

Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.


Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse; ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo.


Ndiloleni, kuti nditsitsimuke, ndisanamuke ndi kukhala kuli zii.


Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?


Koma Yehova akhala chikhalire, anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze.


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri mu Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;


Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa