Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:15 - Buku Lopatulika

15 Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova, ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova, ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Mitundu ya anthu idzalemekeza Chauta moopa, mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopa ulemerero wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova, mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:15
14 Mawu Ofanana  

mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisraele, ndi kuti adziwe kuti nyumba ino ndaimangayi yatchedwa dzina lanu.


Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,


Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m'mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa.


Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.


Mafumu onse a padziko lapansi adzakuyamikani, Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.


Inde mafumu onse adzamgwadira iye, amitundu onse adzamtumikira.


Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.


Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa