Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 102:28 - Buku Lopatulika

28 Ana a atumiki anu adzakhalitsa, ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ana a atumiki anu adzakhalitsa, ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Ana a ife atumiki anu adzakhala opanda nkhaŵa, zidzukulu zathu zidzakhazikika pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu; zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 102:28
14 Mawu Ofanana  

Masiku anu akunga masiku a munthu kodi, zaka zanu zikunga masiku a munthu;


Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse, ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo.


Ndani wachipanga, nachimaliza icho, kutchula mibadwo chiyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pachimaliziro ndine ndemwe.


Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa?


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.


Pakuti monga m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.


Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.


Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa