Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


101 Mauthenga a M’Baibulo Okhudza oledzera

101 Mauthenga a M’Baibulo Okhudza oledzera

Ndikufuna ndikuuzeni lero, ine ndekha, kuti kumwa mowa mopitirira muyezo kungabweretse mavuto ambiri kwa ine ndekha komanso kwa ena. Tiyenera kuganizira za zochita zathu ndi mmene zimakhudzira anthu otizungulira, ndikutenga udindo pa zisankho zathu.

Tikakhala oledzera, tifunika thandizo kuti tipewe zinthu zoopsa. Ndipo zoona zake n'zakuti, kumwa mowa mopitirira muyezo, monga chizolowezi china chilichonse choipa, kungakhale ngati kupembedza mafano. Chilichonse chimene timagwiritsa ntchito m'malo mwa Mulungu kuti tikwaniritse zosowa zathu zamkati chimakhala fano, ndipo chimatipanga akapolo.

Koma lero ndikufuna ndikuuzeni za njira yothawa mavuto amenewa. Mutha kumasuka ku ukapolo wa mowa, ndi mphamvu ya magazi a Khristu. Magazi ake ndi amphamvu zokwanira kukutsukani, kukuchotsani poizoni, ndikukusandutsani munthu watsopano.




1 Akorinto 6:10

kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:18

Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:20

Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 1:5

Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:21

Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:21

Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:36

Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:31

Usayang'ane pavinyo alikufiira, alikung'azimira m'chikho, namweka mosalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 12:25

Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika, ndipo awayendetsa dzandidzandi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:4

Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo; akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:1

Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 1:14

Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:11-12

Tsoka kwa iwo amene adzuka m'mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:20-21

Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:29-35

Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Usakhumbe zolongosoka zake; pokhala zakudya zonyenga. Ngamene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosakanizidwa. Usayang'ane pavinyo alikufiira, alikung'azimira m'chikho, namweka mosalala. Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka, najompha ngati mamba. Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota. Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja, pena wogona pansonga ya mlongoti wa ngalawa. Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; anandikwapula, osamva ine; ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafunafunanso vinyoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:3

Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:8

Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:4-5

Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo; akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti? Kuti angamwe, naiwale malamulo, naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 75:8

Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:34

Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:13-14

Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:11

koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:6-7

Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali, ndi vinyo kwa owawa mtima; amwe, naiwale umphawi wake, osakumbukiranso vuto lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:21

njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:7

Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 10:17

Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:27

Adzandira napambanitsa miyendo ngati munthu woledzera, nathedwa nzeru konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:5

Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:15

Ndidzalingirira pa malangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:37

Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:49

nadzayamba kupanda akapolo anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:45-46

Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera; mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:21

pakuti pakudyaku yense ayamba watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:8

Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza, ndi kutaya mau ako okondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:3

Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:3

Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11

Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:1-3

Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino. Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono. Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa; amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva. Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa. Chifukwa chake imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a mu Yerusalemu. Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga; chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira. Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo. Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kuvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalephereka; popita mliri woopsa udzakuponderezani pansi. Nthawi zonse umapita, udzakutengani; chifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake. Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati chimphepo cha matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu. Pakuti kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi chofunda chachepa, sichingamfikire. Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo. Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi. Tcherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga. Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? Kodi amachocholabe, ndi kuswa zibuma za nthaka? Atakonza thyathyathya pamwamba pake, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza chitowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ake osankhika, ndi mchewere m'maliremo? Pakuti Mulungu wake amlangiza bwino namphunzitsa. Pakuti sapuntha mawere ndi chopunthira chakuthwa, ngakhale kuzunguniza njinga ya galeta pachitowe; koma amakulunga mawere ndi munsi, naomba chitowe ndi chibonga. Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya galeta wake, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ake sapera. Ichinso chifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wake uzizwitsa ndi nzeru yake impambana. Korona wakunyada wa oledzera a Efuremu adzaponderezedwa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:21

Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:7

Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira; koma mnzao wa adyera achititsa atate wake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:23

Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:21

Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru; koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:17

Wokonda zoseketsa adzasauka; wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:24-27

Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire. Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda. Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga; koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:15

Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:5

Mwamuna wanzeru ngwamphamvu; munthu wodziwa ankabe nalimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:13

Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:27

Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa, leka kumva mwambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:27

ndiponso musampatse malo mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:32

Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:4

Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:29

Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi champesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:9

Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:15

Wachibwana akhulupirira mau onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:12-13

Zowindira Inu Mulungu, zili pa ine, ndidzakuchitirani zoyamika. Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa, simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe? Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu m'kuunika kwa amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:19

Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:34

Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:1-3

Pamene ukhala ulinkudya ndi mkulu, zikumbukira ameneyo ali pamaso pako; Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire; ngakhale kulowa m'minda ya amasiye; pakuti Mombolo wao walimba; adzawanenera mlandu wao pa iwe. Lozetsa mtima wako kumwambo, ndi makutu ako ku mau anzeru. Usamane mwana chilango; pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai. Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda. Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa. Imso zanga zidzasangalala, polankhula milomo yako zoongoka. Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse. Pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka. Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, ulunjikitse mtima wako m'njiramo. nuike mpeni pakhosi pako, ngati uli wadyera. Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza. Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amai ako atakalamba. Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha. Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amai ako akondwere, amai ako akukubala asekere. Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga. Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza. Pakuti abisalira ngati wachifwamba, nachulukitsa anthu a chiwembu. Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Usakhumbe zolongosoka zake; pokhala zakudya zonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:17

Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:12

Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:23

Koma iye amene akayikakayika pakudya, atsutsika, chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chilichonse chosatuluka m'chikhulupiriro, ndicho uchimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Woipa akongola, wosabweza, koma wolungama achitira chifundo, napereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:7

amwe, naiwale umphawi wake, osakumbukiranso vuto lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:10

si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m'dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:3

Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake; koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1-2

Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:23

Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:16

Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira, kuti ungakukole, nusanze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:13

Wotseka makutu ake polira waumphawi, nayenso adzalira koma osamvedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:14

monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:23

Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:7

Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:29

Munthu wa chiwawa akopa mnzake, namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:6

pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:27

koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:18

Anavalanso temberero ngati malaya, ndipo lidamlowa m'kati mwake ngati madzi, ndi ngati mafuta m'mafupa ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:23

Masewero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa; koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:5

Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:28

Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 24:9

Iwo sadzamwa vinyo ndi kuimba nyimbo; chakumwa chaukali chidzawawa kwa iwo amene achimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:19-21

Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, ulunjikitse mtima wako m'njiramo. nuike mpeni pakhosi pako, ngati uli wadyera. Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:26

Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:65

Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:19

Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, ulemerero ndi ulemu zikhale zako! Mulungu wanga wakumwamba, Atate Woyera, ndikubwera kwa Inu, podziwa kuti Inu nokha muli ndi Mphamvu yosintha, kuchiritsa, ndi kubwezeretsa moyo wanga. Ndikupemphani kuti mundimasule ku unyolo uliwonse, chomangira, ndi goli la ukapolo lomwe landigwira ku mowa. Masulani moyo wanga ku zikhadabo za mdani, motsogozedwa ndi Mzimu Wanu Woyera, muziphe mwa ine zilakolako za dziko lapansi kuti ndiyambe kuyenda moyo wodalitsidwa. Ndisungeni ndipo mundithandize kudziletsa kuti ndichoke kwa anthu omwe amandilimbikitsa kumwa ndi kuchita machimo awa, kuti ndipite patsogolo ndikubwezeretsa ubale wanga ndi Inu. Chotsani m'maganizo mwanga zilakolako zonyenga za dziko lino, dulani chomangira chilichonse cha moyo wanga, thupi langa, ndipo chotsani m'moyo wanga chilakolako chakumwa. Ndipatseni mphamvu ndi kulimba mtima kuti ndigonjetse zizolowezi zoipa ndikutsatira moyo wanga ndi Mawu anu. Mawu anu amati: "Musaledzere ndi vinyo, momwemo muli kusokonezeka; koma mudzazidwe ndi Mzimu." Atate Woyera, ndikudziwa mkhalidwe wanga, kuti ndakhala moyo wosokonezeka ndipo ndatali nanu, ndikupemphani kuti mundiphunzitse kuyenda mu Mzimu kuti ndisakhutiritse zilakolako za thupi. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa