Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 75:8 - Buku Lopatulika

8 Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 M'manja mwa Chauta mulitu chikho cha vinyo wofanizira chilango chake, vinyo wotutuma ndi wothirako dzoŵaŵa. Adzatsanyula vinyoyo, ndipo oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa, nadzagugudiza mpaka ndungundungu zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 75:8
15 Mawu Ofanana  

Aone yekha chionongeko chake m'maso mwake, namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.


Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.


Chifukwa chake anthu ake amabwera kudza kuno, ndipo chikho chodzala ndi madzi achigugudiza.


Ngamene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosakanizidwa.


Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusakaniza zakumwa zaukali;


Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova chikho cha ukali wake; iwe wamwa mbale ya chikho chonjenjemeretsa ndi kuchigugudiza.


atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ake, Taona, ndachotsa m'dzanja mwako chikho chonjenjemeretsa, ngakhale mbale ya chikho cha ukali wanga; iwe sudzamwa icho kawirinso.


Pakuti Yehova, Mulungu wa Israele, atero kwa ine, Tenga chikho cha vinyo wa ukaliwu padzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.


Ndipo ndinatenga chikho padzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;


Udzamwa ichi ndi kugugudiza, ndi kuchechetachecheta zibade zake, ndi kung'amba mawere ako; pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova.


Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.


Yehova asaukitsa, nalemeretsa; achepetsa, nakuzanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa