Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 55:23 - Buku Lopatulika

23 Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Koma Inu Mulungu mudzaŵaponya adani anga m'dzenje lozama lachiwonongeko. Anthu okhetsa magazi ndi onyenga sadzafika ngakhale theka la masiku ao. Koma ine ndidzadalira Inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipa kulowa mʼdzenje lachiwonongeko; anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengo sadzakhala moyo theka la masiku awo, koma ine ndimadalira Inu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 55:23
19 Mawu Ofanana  

Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Chidzachitika isanadze nthawi yake; pakuti nthambi yake siidzaphuka.


Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.


Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera.


Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, ndisachite manyazi; adani anga asandiseke ine.


Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.


Miphika yanu isanagwire moto waminga, adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.


Iye amene asunga moyo wathu tingafe, osalola phazi lathu literereke.


Indedi muwaika poterera, muwagwetsa kuti muwaononge.


Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.


Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?


Kunsi kwa manda ndi kuchionongeko sikukhuta; ngakhale maso a munthu sakhutai.


Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa