Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 7:34 - Buku Lopatulika

34 Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Mwana wa Munthu adabwera, nkumadya ndi kumwa ndithu, inu mumvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 7:34
13 Mawu Ofanana  

Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?


Ndipo pakulankhula Iye, anamuitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.


Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.


Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nao.


Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.


Ndipo Levi anamkonzera Iye phwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo panali khamu lalikulu la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pachakudya pamodzi nao.


Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda.


Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse.


Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya.


Ndipo anamkonzera Iye chakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye.


Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa