Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


72 Mau a Mulungu Okhudza Nyimbo

72 Mau a Mulungu Okhudza Nyimbo

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, yopangidwa kuti imusangalatse Iye. Inde, Mulungu watipatsa ife talente yoimba, koma gwero la zonse ndi mphamvu zake zazikulu zolenga. M'Mawu a Mulungu, timaona kuti nyimbo zimagwiritsidwa ntchito nthawi yapadera, monga potamanda dzina la Mulungu ndi kukweza ukulu wake, kuvina pamaso pake, kulandira mtendere pakati pa mavuto, ndi kulengeza kugonjetsedwa kwa adani ndi kulengeza chipambano.

Masalimo ambiri analembedwa ngati nyimbo, ena mwa iwo akukhudzana ndi zochitika zenizeni, monga kupambana adani (Eksodo 15.1-18; Oweruza 5.1-31), kutamanda Mulungu, kupempha thandizo kapena chitsogozo. Ndipo kumbukirani, angelo anaimba polengeza kubadwa kwa Yesu (Luka 2.13-14).

Timadziwa kuti mdierekezi wayesa kuwononga tanthauzo la nyimbo, polimbikitsa zoipa ndi chiwerewere, choncho ana a Mulungu ayenera kusunga chiyambi chake ndi kuchiteteza ku machitidwe a dziko lino, lopangidwa ndi Mulungu Wamuyaya.




Aefeso 5:19-20

ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:1-2

Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja. Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza; anamira m'madzi aakulu ngati mtovu. Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa? Mwatambasula dzanja lanu lamanja, nthaka inawameza. Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; mwamphamvu yanu mudawalondolera njira yakunka pokhala panu poyera. Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; kuda mtima kwagwira anthu okhala mu Filistiya. Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala mu Kanani onse asungunuka mtima. Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola. Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika. Yehova adzachita ufumu nthawi yonka muyaya. Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:3

Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:1-2

Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu. Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga. Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:1

Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 5:3

Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu; ndidzamuimbira ine Yehova, inetu; ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 45:1

Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 16:23

Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:13

Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 13:8

Ndipo Davide ndi Aisraele onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 105:2

Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:33

Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 57:7

Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:19

ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 15:16

Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:2-3

Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi. Moyo wathu walindira Yehova; Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu. Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera. Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife, monga takuyembekezani Inu. Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano; muimbe mwaluso kumveketsa mau.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:9

Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:23

Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 23:5

ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:2

Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:23-25

Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu, zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 38:20

Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 5:13

Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 12:27

Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti achite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 29:30

Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 87:7

Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati, akasupe anga onse ali mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 34:12

Ndipo amunawo anachita ntchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yahati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena aliyense waluso la zoimbira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 3:11

Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:1

Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 108:1-3

Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga. Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu? Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya osatuluka nao magulu athu? Tithandizeni mumsauko; pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa. Galamukani, chisakasa ndi zeze; ndidzauka ndekha mamawa. Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:4

mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:1-3

Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza. Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu. Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo. Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha. Yehova apenyerera m'mwamba; aona ana onse a anthu. M'malo akhalamo Iye, amapenya pansi pa onse akukhala m'dziko lapansi. Iye amene akonza mitima ya iwo onse, amene azindikira zochita zao zonse. Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa, mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona. Kavalo safikana kupulumuka naye, chinkana mphamvu yake njaikulu sapulumutsa. Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake. Kupulumutsa moyo wao kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala. Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi. Moyo wathu walindira Yehova; Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu. Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera. Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife, monga takuyembekezani Inu. Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano; muimbe mwaluso kumveketsa mau.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:3

Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:4

Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:4

Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 81:1-2

Imbitsirani Mulungu ndiye mphamvu yathu; fuulirani kwa Mulungu wa Yakobo. Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukuchotsa kudziko la Ejipito; yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza. Koma anthu anga sanamvere mau anga; ndipo Israele sanandivomere. Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao. Ha! Akadandimvera anthu anga, akadayenda m'njira zanga Israele! Ndikadagonjetsa adani ao msanga, ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa. Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga, koma nyengo yao ikadakhala yosatha. Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa, ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m'thanthwe. Utsani salimo, bwera nakoni kalingaka, zeze wokondwetsa pamodzi ndi chisakasa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:1-3

Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano. Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira. Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri, kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse. Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 43:4

Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:3

Koma Inu ndinu woyera, wakukhala m'malemekezo a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:1-2

Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika. Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake. Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera. Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi. Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 5:13-14

Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova; ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 98:4-6

Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze; ndi zeze ndi mau a salimo. Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova, ndi mbetete ndi liu la lipenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:1-2

Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 61:8

Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:1

Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:9

Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu; pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:11-12

Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero, kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:1

Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:1-2

Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga. Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:7

Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe; muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:30

Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru, ndi lilime lake linena chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:1-3

Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao. Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 150:1-6

Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 5:9

Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:5

Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:54

Malemba anu anakhala nyimbo zanga m'nyumba ya ulendo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:10

ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:3

Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 52:8-9

Mau a alonda ako! Akweza mau, aimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni. Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:12-13

Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni. Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 6:5

akungoimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoimbira nazo ngati Davide;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:30

Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:25

Koma mwana wake wamkulu anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuimba ndi kuvina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:25

Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:9

ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:15

Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:12

Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:15

Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 5:8-9

Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima. Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:2-3

Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao; Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi. ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 15:2-3

Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosakaniza ndi moto; ndipo iwo amene anachigonjetsa chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu. Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Wamuyaya, Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu wokongola pa moyo wanga, ndili ndi mwayi woti ndikuimbireni nyimbo zanga zachikondi ndi kulambira kwanu. Atate, munalenga zonse ndi cholinga, ndipo cholinga chake ndicho kuti dzina lanu lilemekezeke, likwezeke, ndipo nyimbo ndi njira imodzi yochitira zimenezo. Ndithandizeni kukhala wolambira woona, wotsogoleredwa ndi Mzimu Woyera wanu, kuti chofunika kwambiri pa moyo wanga chikhale kukusangalatsani, kuphatikizapo zonse zomwe makutu anga akumva. Munditeteze kuti ndisagwere m’chinyengo cha kukondedwa ndi kunyengereredwa ndi nyimbo za dziko. Ndithandizeni kusamala pa zinthu zonsezi ndipo ndisamvere nyimbo zomwe mawu ake sandilimbikitse. Ndikupemphani kuti mawu anu akhale ochuluka m’moyo mwanga, kuti chinthu chamtengo wapatali kwambiri kwa ine chikhale kukhala nanu pafupi. Sungani maganizo anga ndi mtima wanga kuti ndikhale ndi mzimu wopanda chilema ndipo ndikusangalatseni kudzera m’nyimbo, zitamando, ndi kulambira. Mawu anu amati: “Mulankhulane wina ndi mnzake ndi masalmo, ndi nyimbo, ndi nyimbo zauzimu, muimbire ndi kutamanda Ambuye mumtima mwanu.” Ambuye, ndikupemphani kuti zitamando zikhale ndi mphamvu pa miyoyo ya achinyamata, anyamata ndi atsikana, amayi ndi abambo. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa