Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 10:1 - Buku Lopatulika

1 Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chifukwa chiyani mumaima kutali nafe, Inu Chauta? Chifukwa chiyani mumabisala pamene tili pa mavuto?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali? Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 10:1
13 Mawu Ofanana  

Mubisiranji nkhope yanu, ndi kundiyesa mdani wanu?


akachita Iye kulamanzere, sindimpenyerera; akabisala kulamanja, sindimuona.


Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?


Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.


Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu; munabisa nkhope yanu; ndinaopa.


Mubisiranji nkhope yanu, ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?


Pakuti moyo wathu waweramira kufumbi, pamimba pathu pakangamira dziko lapansi.


Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.


Yehova mutayiranji moyo wanga? Ndi kundibisira nkhope yanu?


Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?


Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa